Malawi Broadcasting Corporation
Business Local Local News Nkhani

‘Sugar tsopano alipo ochuluka’

Anthu ambiri munzinda wa Blantyre ati ndi okondwa kwambiri kaamba kakuchuluka kwa sugar yemwe akupezeka m’masitolo komanso malo ochitira malonda ambiri.

Pakadali pano, mtengo wa sugar ukutsika komanso kukhazikika poyerekeza ndi momwe zinthu zinaliri masiku angapo apitawa chifukwa tsopano akugulitsidwa pa mitengo yapakati pa K2800 ndi K3000.

Chopatsa chidwi ndi chakuti ena mwa anthu ochita malonda omwe akhala akugulitsa sugar kunja kwa sitolo zina zikuluzikulu nawonso atsitsa mitengo yawo.

A Mirriam Chiwalo, amene amakhala ku Manyowe munzinda wa Blantyre, anati: “Panopa palibe kuchitira mwina koma kugulitsa sugar pa mtengo wa K3000 chifukwa choti wabwera wambiri mu sitolo ina yayikulu yomwe takhala tikumakagula ndi cholinga choti tidzigulitsanso kwa anthu ena.

“Zinthu tsopano zili bwino ndipo ndi zosangalatsa kwambiri kuti palibenso zokanganirana sugar monga momwe zinaliri padzana paja,” a Chiwalo adatero.

Posachedwapa, mkulu wa kampani ya Illovo Sugar, a Kondwani Msimuko, adanenetsa kuti katunduyu ayamba kupezeka mochuluka potsatira kuyambiranso kwa nyengo yogaya sugar.

Related posts

Five TAs in Thyolo improve on hygiene

MBC Online

Chinese firm to establish US$100 million EV plant in Nigeria

MBC Online

CHAKWERA SECURES K32 BN FOR GOLOMOTI SOLAR POWER PLANT

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.