Othamanga amene akapikisane ku mpikisano wa Blantyre 42.195 Kilometres awachotsera ndalama zimene amayenera kulipira kuti atenge nawo gawo.
Wapampando wa komiti yomwe ikuyendetsa mpikisanowu, a Limbani Matola, amenenso ndi mkulu wa zamalonda ku nthambi ya Malawi National Council of Sports, ati apanga izi ndi cholinga chopereka mwayi kwa othamanga onse, kuphatikizapo omwe ndi ochepekedwa, kuti atenge nawo mumpikisanowu.
Othamanga mtunda wa makilomita 42.195 amayenera kumalipira K20,000 pomwe a mtunda wa makilomita khumi amayenera kulipira ndalama zokwana K15,000 kuti akapikisane nawo.
Wapampando wa bungwe loyendetsa masewero othamanga m’dziko muno, a Kondwani Chamwala, anayamikira nthambi ya Sports Council kaamba ka ganizolo ndipo ati izi zilimbikitsa ochita masewerowa kulimbikira kusula luso lawo.
Mpikisanowu uchitika loweruka lino ndipo udzayambira ndi kuthera pa bwalo la Kamuzu.
Olemba: Amin Mussa