Mai Fanny Dyson Banda akufuna thandizo kuti mwana wawo yemwe ali ndi vuto mmutu akalandire thandizo lamankhwala kuchipatala cha gulupu ku Blantyre.
Mwanayu anabadwa pa 2 April, 2023.
Ma Banda ati mwana wawo yemwe ndi wamkazi ali ndi vuto lakutsekeka kwa misempha yodutsa madzi mmutu ndipo anamuchita opaleshoni ndikuika paipi mmutumo zomwe zimachititsa kuti adzipita pita kuchipatala cha gulupu.
Panopa maiwa akufunika apitenso kuchipatalako kuti madotolo akamuone mwanayo ngati paipiyo ikugwira bwino ntchito komanso ngati ndi kofunika kuti ayichotsemo, koma vuto lomwe ali nalo ndimayendedwe kuchoka ku Mangochi kupita ku Blantyre komanso zina ndi zina zowathandizira paulendo umenewu poganizila kuti akafika kuchipatalako amakhalako masiku angapo.
“Amuna anga anandithawa kale kale ananena kuti sangwanitse kotelo ndilibe munthu oti andithandize,” atero mai Banda.