Bwalo la High Court Ku Lilongwe lagamula kuti a Anne Mumba ndi wolakwa pamlandu woti ndiwo adapha amuna awo, malemu Professor Peter Mumba.
Justice Mzondi Mvula ndiye wapereka chigamulochi, pambuyo potsatira zikalata zonse zamlandu kwa maola pafupifupi anayi.
Justice Mvula wati a Anne Mumba adachita dala zimenezi pomwe adasunga thupi la Professor Mumba m’nyumba ponena kuti momwe amaimbira foni anthu nkuti atamwalira kale ndipo panali patatha maola awiri.
Bwalo linatsutsanso kuti Malemu Mumba amkakana kupita kuchipatala pomwe mbili yawo imaonetsa kuti amapita kuchipatala chifukwa cha vuto lawo lakuthamanga kwa magazi.
Professor Mumba, omwe anali atapuma pa ntchito, analemba bukhu komanso kumanga nyumba, zomwe Justice Mvula anati zimaonetsa kuti sakanakana kupita kuchipatala chifukwa amafunabe moyo.
Pakadali pano, Justice Mzondi Mvula wati a Anne Mumba khalidwe lao laonetsa poyera kuti amafuna amuna awo atafa pofuna chuma.
Iwo ati pochoka msanga kumudzi tsiku lomwe adaika maliro, zinaonetsanso poyera zamalingaliro amayiwa.
Pali chiyembekezo choti chigamulo cha mlandu chikhoza kudzaperekedwa pa 25 July chaka chomwe.chino.
Mubwaloli, a Anne Mumba analira kwambiri, chimodzimodzi akuchimuna, omwe amati chilungamo chadziwika.