Mafumu a m’boma la Blantyre ayamikira boma pokhazikitsa ntchito yolembetsa umwini wa malo.
Mfumu yayikulu Kunthembwe inati ntchito yolembetsa maloyi ndi yabwino kwambiri kaamba kakuti ichepetsa ziwawa zimene zimabwera chifukwa cha kusamvana pa nkhani zokhudza malo.
Iwo amayankhula izi pa msonkhano wapakati pa unduna wa zamalo ndi mafumu okhala m’mbali mwa mtsinje wa Shire.
Mkulu oona za zantchito kuunduna wa zamalo, a Dr Victor Sandikomda, anati mafumu ndi ofunika kuti amvetse bwino malamulo atsopano a malo chifukwa iwo ndi eni nthaka.
Ntchitoyi ikutheka ndi thandizo lochokera ku bungwe la Malawi Watershed Services Improvement Project.