Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

MEC ionjezera masiku m’gawo loyamba la kalembera

Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) lati lionjezera masiku mu kalembera wachisankho m’gawo loyamba.

Chikalata chomwe wasainira wapampando wa bungweli, Justice Annabel Mtalimanja, chati MEC yachita izi kaamba koti panalibe ogwira ntchito a bungwe la National Registration Bureau (NRB) malo olembetsera voti pamene khothi linalamula pa 25 October mwezi uno kuti malo onse olembetserawo mukhale a NRB.

MEC yati  izi sizisokoneza kalembera wagawo  lachiwiri poti bungwelo lipitilira ndi gawolo monga analengezera.

Mchikalatacho, a Mtalimanja ati MEC ikumana ndi bungwe la  NRB kuti atsatire chigamulo chomwe akhoti anapereka kuti anthu omwe akufuna kulembetsa chiphatso cha unzika athe kutero malo olembetsera voti.

 

Olemba: Austin Fukula

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Anayi awamanga ataba zipangizo za galimoto

Charles Pensulo

US citizen constructs K43 million slab road

MBC Online

Pali kusintha kwina pa programme — Kunkuyu

Beatrice Mwape
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.