Osewera wakale wa timu ya pfuko lino, Flames, Chimango Kayira, wati akukhulupilira kuti masewero apakati pa South Africa ndi Malawi, amene alipo masanawa pa bwalo lamasewero la Loftus munzinda wa Pretoria, akhala ngati masamu.
MBC ikupatsirani tsatanetsatane wa masewerowa pa MBC TV 1, 2ontheGo, komanso Radio 2 FM.
Masewerowa ndi achibwereza amumpikisano odzigulira malo ku 2024 TotalEnergies CAF African Nations Championship (CHAN) pamene Malawi idakutha South Africa 1-0 kudzera mu chigoli cha Zeliati Nkhoma pa mphindi 87 pa bwalo lamasewero la Bingu National munzinda wa Lilongwe.

“Ndikutha kuoona aphunzitsi a mayiko awiriwa akuchita kasinthasintha wa kaseweredwe komanso osewera masewerowa ali mkati chifukwa awa ndi masewero odzigulira malo,” iye adatero.
Wachiwiri kwa mphunzitsi wa Flames, Peter Mponda, naye adati masewerowa akhala ovuta zedi.
“Tawakonzekera mokwanira, koma mu mphindi 10 kapena 15 zoyambilira, anzathuwa akhala akufuna chigoli. Mudziwetu kuti ichi ndi chigawo chachiwiri ndipo tisatayilire,” iye adatero.
Popita kumasewerowa, Mphunzitsi wa South Africa, Molefi Nseki, wayitanitsa osewera oonjezera asanu ndi m’modzi koma Mponda adati izi sizikuwasuntha.

Chifukwa Malawi idapambana 1-0 m’masewero oyambilira, ndiye kuti ikhoza kupitabe ku CHAN ngakhale itagonja 1-0, malinga ndi malamulo amene amawatcha kuti ‘Away Goal’.
M’masewero odzigulira malo kumpikisanowu oyambilira, Malawi idathambitsa Comoros 4-0, itawapambadza zigoli ziwiri kwa chilowere m’masewero awiri koyenda komanso pakhomo.
Mbali inayi, South Africa idapweteka Egypt 4-2, itagonjetsa ana a Farao 3-1 pakhomo pawo ndi kufanana mphamvu 1-1 pakhomo pa Bafana Bafana.
Mpikisano wa 2024 CHAN, umene osewera ake ndi amene amasewera m’matimu amayiko awo ndipo Malawi sidayambe yapitako, udzachitikira m’mayiko a Kenya, Tanzania, and Uganda kuyambira pa 2 mpakana pa 30 August chaka chino.