Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

Malizani msewu mu nthawi yake — PAC

Wapampando wa komiti ya Public Accounts a Mark Botomani ati ndi okhumudwa kaamba ka kuchedwa komaliza kwa ntchito yokonza msewu wa pa Kammwamba.

Msewuwu ndi otalika makilomita asanu ndi imodzi ndipo uli mbali imodzi yakonzanso msewu wa Zalewa kupita kwa Chingeni m’boma la Balaka, omwe ndi otalika makilomita pafupifupi 65.

Izi zikutsatira zokambirana zomwe a Road Fund Administration anachita ndi komitiyi zokhudza msewuwu.

Kontalakitala yemwe akukonza msewuwu wati mwa zina, kutsika mphamvu kwa ndalama ya klKwacha ndi kumene kwachedwetsa ntchitoyi.

Poyankhula atawuyendera, a Botomani anati afikanso pa malopa pakadutsa miyezi itatu pamene akaone m’mene ntchitoyi ikuyendera pomwe nthawi yake yomwe anakonza kuti ukhale utatha yadutsa.

Wapampando wa bungwe la National Roads Fund Administration, a Matthews Chikakheni, anatsimikiza kuti ndalama zogwilira ntchitoyi zilipo ndipo a Malawi asade nkhawa poti ntchitoyi yayambilanso ndipo makontalakitala atsimikiza kuti itha nyengo ya mvula isanafike.

Ntchitoyi inayamba m’mwezi wa July cha chatha ndipo imayembekezeka kutha mwezi uno.

Olemba: Naomi Kamuyango

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Govt hails elderly rights promotion efforts

Secret Segula

MCP, UTM STRENGTHEN TIES

McDonald Chiwayula

DIOs to champion awareness on 2063 agenda

Timothy Kateta
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.