Maiko a Malawi ndi Tanzania akuchita nawo mwambo okondwerera tsiku la chiyankhulo cha Kiswahili munzinda wa Lilongwe.
Mwambowu umachitika pofuna kulimbikitsa umodzi pakati pamaiko komanso chikhalidwe choyankhula ziyankhulo zosiyanasiyana pakati pa anthu.
Ena mwa amene ali kumeneku ndi monga kazembe wa dziko la Tanzania kuno ku Malawi, a Agness Kayola ndi nthumwi zawo.
Wachiwiri kwa kazembe wa dziko la Zimbabwe alinso komweku pamodzi ndi akuluakulu amu unduna owona za ubale wadzikolino ndi maiko ena, kuphatikizaponso ophunzira pa sukulu za ukachenjede.