Mtsogoleri wadziko lino, Dr Lazarus Chakwera, lero akuyendera ntchito zosiyanasiyana zachitukuko m’boma la Mangochi.
Kuchoka apo, Dr Chakwera ayendera ntchito yomanga ofesi yatsopano ku khonsolo ya Mangochi, ntchito yomwe boma likugwira mogwirizana ndi dziko la Iceland.
Kenako, Dr Chakwera afika ku Monkey Bay, kumene ayenderenso ntchito ya msewu wa Monkey Bay – Cape Maclear- T378 mdera la mfumu yaikulu Nankumba.
Olemba: Owen Mavula