Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

MAKHANSALA AWIRI A DPP ALOWA MCP KU PHALOMBE

Makhansala awiri a chipani cha Democratic Progressive (DPP) atuluka mchipanichi  ndipo alowa cha Malawi Congress (MCP).

Mkulu okopa anthu mu MCP a Moses Kunkuyu  alandila makhansala awiriwa pa msonkhano omwe anachititsa pa sukulu ya Chilayeni m’dera la Sub TA Nyambalo ku Phalombe.

Makhansalawa ndi a Felix Blair Jumbe a Mauzi ward mdera la Phalombe North East, komanso a Fedison Thomas a dera la Likulezi Ward kum’mwera kwa Phalombe.

Makhansalawa omwe anabwela ndi mafumu a m’maderawa ati achita izi kaamba Prezidenti Dr Lazarus Chakwera ndi okhululuka komanso chipani chawo ndi cha mtendere ndipo akufuna chitukuko.

 

Related posts

Nzika ya Niger akuyisunga ku Maula

Romeo Umali

TNM ipereka mabandulo aulere kwa makasitomala ake popilira kuvuta kwa internet

Romeo Umali

Anthu aku Nsalu ku Lilongwe awalangiza kuti akavotere Dr Lazarus Chakwera pa chisankho cha chaka chino kuti zitukuko zipitilire.

Mayeso Chikhadzula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.