Mayi wa dziko lino, Madam Monica Chakwera, wapempha mafumu m’dziko muno kuti athandize kuwongola ana m’madera mwawo, powalimbikitsa sukulu m’malo mwa ukwati ndikuwazindikiritsa kuyipa kochita mchitidwe ogonana akadali achichepere.
Mayi wa dziko linoyu wanena izi ku Bingu International Convention Centre ku Lilongwe pa mkumano umene anakonzera mafumu akuluakulu a m’dziko muno kuti akambirane za momwe angathandizire kuchepetsa mimba zosakonzekera pakati pa atsikana komanso ukwati wa ana achichepere.
Madam Chakwera ati mafumuwa ali ndi udindo owateteza anawa, maka pakaganizidwe, potengera ndi zimene amamva komanso kuonera m’madera omwe akukhala.
Mayi wa dziko linoyu wati chiwerengero cha atsikana omwe akutenga mimba, kukwatiwa, kumwalira, komanso kukhala pa chiopsezo cha cancer ya khomo la chiberekero chikadali chokwera choncho nkofunika kugwirana manja pothandiza anawa kuti mavutowa achepe.
Pa mwambowu, Inkosi ya Makosi M’belwa yawerenga chikalata cha zomwe mafumuwa agwirizana polimbana ndi mimba komanso ukwati wa ana, zomwe mwazina ndi kukhazikitsa malamulo othandizira kuchepetsa mimba komanso ukwati wa ana, kugwiritsa ntchito zilango zofanana.