Bungwe la Tobacco Commission lalangiza alimi a fodya m’dziko muno kuti ayambiretu ku konzekera ulimi wa fodya wa chaka cha mawa chifukwa kuzula mwachangu fodya wakale kumachepetsa matenda ndi tizilombo m’munda akabzyalamo fodya watsopano.
Ofalitsa nkhani ku bungweli, a Telephorus Chigwenembe, ndi amene anapereka langizoli pamene amazindikiritsa alimi zakufunika kozula mitengo yakale ya fodya.
A Thomson Chiwaya, amene ndi m’modzi mwa alimi a fodya, amene amakhala kwa Nyezelera m’boma la Phalombe, anati iwo anachotsa kale mitengo ya fodya ya chaka chino pokonzekera ulimi wachaka cha mawa.
Nawo a Weston Majiya, omwenso ndi mlimi wa fodya, ati ayambapo kale kusosa minda yawo ya fodya popeza alimbikitsika ndi mitengo yogulitsira fodya yomwe inaliko ku msika wa chaka chino.