Mkulu wa kampani ya Magic promotions, a Brazio Mathias, ati chilichonse chikuyenda bwino pamene akukonzekera kuti aonetse koyamba kwa aMalawi kanema wawo otchedwa “Justice” amene anamukonza ndi cholinga chofuna kuthetsa m’chitidwe ozembetsa anthu.
Iwo ati aMalawi awonere kanemayu kaamba kakuti awatsegula m’maso.
“Tisanamizane kuti mchitidwewu sukuchitika m’dziko muno. Ngati sizinakuonekere usatase kwambiri. Kanemayi tamupanga kuti tidziwitse anthu za kuipa kwamchitidwe umenewu,” anatero a Mathias.
Iwo anati ayambira kuonetsa anthu a munzinda wa Lilongwe pa 26 July asanaite m’zigawo zina.
Ena mwa akatswiri amene ali mu kanemayu ndi monga Dorothy Kingston ndi Joyce Chavula Mhango.