Malawi Broadcasting Corporation
Agriculture Development Local Local News Nkhani

Greenbelt yagulitsa matumba opyola 3,000 ku NFRA

Bungwe la Greenbelt Authority lagulitsa matumba a chimanga okwana 3,300 ku nkhokwe za bungwe la National Food Reserves Agency (NFRA).

Mkulu wa Greenbelt Authority, a Eric Chidzungu, ati cholinga chawo ndi kuonetsetsa kuti akuthandiza dziko lino kukhala ndi chakudya chokwanira.

A Chizungu anati iwo akufuna kuonjezera malo amene akuchitapo ulimi wa m’thilira m’boma la Chikwawa kuti mu zaka zikubwerazi, chakudya chidzipezeka mosavuta.

A Cosmas Perekani, m’modzi mwa akuluakulu a bungwe la NFRA, anati iwo ndi okondwera kuti magulu ambiri ali ndi chidwi chogulitsa chimanga chawo ku bungweli.

A Perekani ati akuyembekeza kugula matani okwana 120,000 a chimanga ndipo matani okwana 60,000 achoka kwa alimi omwe anachita nawo m’gwirizano ndipo ina ichokera kwa alimi ena amene ali ndi chimanga m’dziko muno.

Matumba 3,300 amene awagulitsa ku NFRA anawakolola pa munda wa mahekitala 100 omwe ndi wa bungweli.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

ACB CLARIFIES ON MISSING DOCUMENT

McDonald Chiwayula

‘Mangani ofesi zoti anthu awulumali apeze thandizo mosavuta’

Austin Fukula

US – IRELAND COMMIT $17 MN FOR STRENGTHENING FOOD SYSTEMS

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.