Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Michael Usi, watsindika kufunika kwa mgwirizano wabwino pakati pa atsogoleri amabungwe omenyera ufulu wa anthu komanso boma pa ntchito yoteteza ndi kulimbikitsa ufulu.
Dr. Usi anena izi m’boma la Mangochi pamwambo okondwelera tsiku la ufulu pa dziko lonse umene umachitikira pa bwalo la masewero la m’bomalo.
Iwo anati boma limazindikira kufunika kwa ntchito imene mabungwe omenyera ufulu wa anthu amagwira poteteza ndi kulemekeza ufulu wa chibadwidwe.
Komabe, a Usi anati chofunika kwambiri ndi kulimbikitsa mgwirizano pakati pambali ziwirizi.
Dr Usi anapereka chitsanzo kuti pamene mabungwe omenyera ufulu wa anthu ali ndi nkhawa kapena madandaulo adzigwiritsa ntchito ndondomeko zoyenera monga kukambirana asanathamangire kumsewu kukachita zionetsero.
Wapampando wa bungwe la Malawi Human Rights Commission, a Chikondi Chijozi, anati m’zaka makumi awiri ndi zisanu zapitazi, bungweli layesetsa kulimbikitsa ntchito yoteteza ufulu wa anthu m’magawo onse ofunikira.
Olemba: Owen Mavula