Malawi Broadcasting Corporation
Crime Local Local News Nkhani

Ali m’chitokosi pobaya ofisala wapolisi

Apolisi m’boma la Mangochi amanga a Arnold Moyowatha, 54, powaganizira kuti anabaya pamimba wapolisi pamene amafuna kuti awamange.

Ofalitsa nkhani za apolisi m’bomali, a Amina Tepani Daudi, ati izi zinachitika pamene apolisi anali pa ntchito yawo yoyendera m’madera amene kumachitika umbanda ndipo a Moyowatha anali ndi anzawo ena awiri amene anathawa.

A Daudi ati pamene a Moyowatha amafuna kuti adzipulumutse anatulutsa mpeni ndi kuvulaza wapolisiyo amene anathamangira naye kuchipatala ndipo anakalandira thandizo.

A Moyowatha ali m’chitokosi pamene akudikira kukaonekera kubwalo la milandu.

 

Related posts

Chawinga sisters in Scorchers’ strong COSAFA squad

Romeo Umali

MERA CAUTIONS ON ILLEGAL FUEL VENDING AND HOARDING

MBC Online

MANEPO hails President Chakwera for endorsing Elderly Bill

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.