Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

CTS Courier yati ikufuna kupereka mwayi watchito kwa achinyamata

Akuluakulu akampani yonyamula katundu ya CTS ati akufunitsitsa kupereka mwayi watchito kwa achinyamata pomwe ali ndimalingaliro owonjezerabe ofesi zawo mzigawo zonse mdziko muno.

Mkulu wa kampaniyi Jacqueline Bokosi wati akufuna kupereka chitsanzo kwa achinyamata ena kukhala ndi chidwi komanso kulimbikira pa bizinezi zawo ndikuthandiza achinyamata anzawo.

Bokosi wayankhula izi kutsatira kukhazikitsa kwa ofesi zina zatsopano za kampaniyi ku Mponela, Dowa komanso ku Area 25 ndi Area 18 ku Lilongwe.

Mmodzi mwa achinyamata yemwe adalembedwa ntchito ndi kampaniyi ndipo tsopano akuyang’anira ofesi ya tsopano ku Area 18, Angel Kabango, wati moyo wake unasintha kwambiri ndipo akukwanitsa kupeza zosowa za pabanja lake.

Kampani ya CTS inayamba mchaka cha 2021 ndipo ili ndi ofesi pafupifupi makumi awiri mzigawo zonse mdziko muno

 

Olemba: Foster Maulidi

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

‘Andale asamalowelere ntchito zam’ma khonsolo’

Charles Pensulo

Muslims hold Eid Ul Fitr prayers

Jeffrey Chinawa

‘Boma likukumana ndi zovuta polimbana ndi mchitidwe wa nkhanza kwa anthu achikulire’

Beatrice Mwape
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.