Bungwe la Football Association of Malawi (FAM) lati mpikisano wa Airtel Top 8 uyamba pa 14 September chaka chino pamene FCB Nyasa Big Bullets ndi timu ya Civil Service United adzakumane pa bwalo lamasewero la Kamuzu ku Blantyre.
Pa 15 September, matimu a Mighty Mukuru Wanderers ndi Bangwe All Stars adzachotsana chimbenene
pa bwalo lomweli pomwe Chitipa United idzakumana ndi Kamuzu Barracks pa bwalo lamasewero la Karonga.
Ndipo p 18 September, Silver Strikers idzasewera ndi timu ya Premier Bet Dedza Dynamos pa bwalo lamasewero la Silver ku Lilongwe.
Matimuwa adzakumananso pakadzadutsa masiku khumi m’masewero achibwereza amene adzangosinthama mabwalo ndipo kumeneko kudzakhala kukwangula gawo loyamba la ndime ya kapherachoka.
Gawo la matimu anayi otsala lidzakhalapo pa 26 ndi pa 27 m’mwezi wa October, koma mu ndimeyi sikudzakhala masewero achibwereza.
Muchikalata cha FAM chomwe taona, mpikisanowu ukuyenereka kutha pa 3 November chaka chino patachitika masewero khumi ndi amodzi.
Opambana adzatenga chikho ndi ndalama yokwana K30 million, yachiwiri yake idzatenga K10 million ndipo ma timu onse otenga nawo gawo adzatenga K2.5 million.
Katswiri omwetsa zigoli zambiri adzapatsidwa K1.5 million, pamene osewera bwino m’chikhochi adzalandira K1 million komanso osewera bwino m’masewero ena aliwonse adzidzalandira K 100 thousand.
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets ndi imene ikusungira chikho cha mpikisanowu.