Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Chikho cha K10 million achikhazikitsa m’boma la Chikwawa

Mmodzi mwa makhumutcha  ochita malonda kwa Ngabu m’boma la Chikwawa Saeed Dinyelo lero wakhazikitsa chikho cha mpira wa miyendo cha ndalama zokwana K10 million.

Mwambowu unachitikira pa bwalo Ngabu Community m’bomalo.

Mmawu ake,  Dinyelo anati wachita izi pamene  ali ndi masomphenya oti derali lidzatulutse timu yomwe idzasewerere mu TNM Super League mtsogolomu.

Mmodzi mwa akuluakulu a bungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo mdziko muno la FAM, a Daud Mtanthiko ayamikira a Dinyelo pothandizira kupititsa patsogolo masewerowa mdziko muno.

Phungu wa chipani cha MCP wa  delari a Illias Karim anali nawonso pa mwambowu

Matimu okwana 32 ndi omwe atenge nawo mbali mu mpikisanowu.

Pamasewero okhazikitsa chikhochi, timu ya Mapoliko yagonjetsa  Chimpambana Red Tigers ndi zigoli zitatu kwa ziwiri.

 

Olemba Nobert Jameson

Related posts

UNFPA GIVES NSO K60M WORTH ICT GADGETS

Rabson Kondowe

We got you covered — NEEF

Romeo Umali

Poverty rate falls as Government launches Sixth Household Survey Report

McDonald Chiwayula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.