President Dr Lazarus Chakwera wathokoza Sinodi ya Livingstonia ya mpingo wa CCAP chifukwa chothandiza boma pa ntchito zosiyanasiyana za chitukuko.
Poyankhula pa mwambo wa mapemphero womwe ukuchitika pa mpingo wa Mchengautuba ku Mzuzu, a Chakwera ayamikira kuti sinodi ikuthandiza mu nthambi za maphunziro, ukhondo komanso kuthetsa njala m’dziko muno.
Iye wati ichi ndi chizindikiro chakuti mpingowu ndi wodzipereka pofuna kuonetsetsa kuti masomphenya a dziko lino a mlozo wa 2063 akwanilitsidwa.