Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani

Chakwera wafika m’dziko la UAE

Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera ndi Madam Monica Chakwera ali ku Abu Dhabi m’dziko la United Arab Emirates (UAE) kumene achite zokambirana ndi mtsogoleri wa dzikolo, Sheikh Mohammed Bin Zayed Alhyan, pankhani zothandiza kuthetsa vuto lakusowa kwa mafuta agalimoto m’dziko muno.

Dr Chakwera afikira pa bwalo la ndege la Al Bateen Executive ndipo analandiridwa ndi kazembe wa dziko la Malawi m’dziko la Kuwait komanso akuluakulu a boma la UAE.

Sheikh Alhyan ndi amene anayitana Dr Chakwera kuti achite zokambiranazi.

Dziko la UAE ndi limodzi mwa mayiko amene chuma chawo chinakwera kwambiri kaamba kodalira ntchito zoyenga mafuta, zokopa alendo komanso ulimi wa minda ikuluikulu.

Olemba: Jackson Sichali, Abu Dhabi, UAE

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Experts should guide on crop alternatives –Meteorologist

Earlene Chimoyo

Tigwirane manja potolera ndalama zoyendetsera ligi — SULOM

Emmanuel Chikonso

Titsegula misewu-yi pofika December chaka chino — Hara

Beatrice Mwape
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.