Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera komanso mayi wa dziko lino Madam Monica Chakwera, alembetsa mu kaundula wa voti pa sukulu ya Malembo m’boma la Lilongwe.
Dr Chakwera ndi mai wa dziko linoyu alembetsa mu kaundulayu pomwe akuchititsa misonkhano yoimaima yomemeza anthu kuti alembetse mkaundulayu m’boma la Lilongwe.
Atalembetsa mu kaundulayu, Mtsogoleri wa dziko linoyu walimbikitsa a Malawi onse kuti atengelepo chitsanzo pokalembetsa mu kaundulayu poti ati ndi ufulu wawo ndipo akatelo zidzawapatsa mphamvu yodzaponya voti pa chisankho cha chaka cha mawa.
Bungwe la MEC linatsegulira gawo lachitatu lolembetsa mu kaundulayu lomwenso ndi lomaliza 28 November ndipo lidzatha pa 11 December.