Bungwe la Malawi Red Cross Society lapeleka ndalama zokwana K250,000 kwa mabanja okwana 724 ku Karonga ngati thandizo kutsatira ngozi ya kusefukira kwa madzi yomwe idasautsa bomali.
Zikaonkhetsedwa, ndalamazi zikukwana K180 million.
A Luis Solomon, amene ndi m’modzi mwa akuluakulu a bungweli, ati apeleka thandizolo kuti anthuwa amangenso nyumba zawo.
“Ndalamazi tagawa kwa anthu ochokera Madera a Mwilang’ombe, Kyungu ndi Kilupula,” anatero a Solomon.
Madzi ochoka mitsinje ya Lufilya, Kyungu ndi North Rukuru anasefukira, zimene zinaachititsa kuti nyumba, ziweto ndi katundu wambiri, kuphatikizapo chakudya, zikokoloke.
Olemba: Hassan Phiri
#MBCDigital
#Manthu