Katswiri oyimba nyimbo za chamba cha Reggae, Burning Spear, wapereka gitala yake imene wakhala akuyigwiritsa ntchito kwa nthawi yayitali kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera, ngati mphatso.
Lachisanu, oyimbayu anakaonekera kwa Dr Chakwera ku Kamuzu Palace munzinda wa Lilongwe ndipo anati ndi okondwa.
Mtsogoleri wa dziko linoyu anauza katswiriyu kuti wakhala akutsatira nyimbo zake kwa nthawi yaitali chifukwa ndi zolimbikitsa chilungamo, bata komanso kumenyera ufulu.
Burning Spear ayimba Loweruka lino pa bwalo la Civo munzindawu.
Olemba: Isaac Jali