Mkhalakale pa nyimbo za Reggae wa mdziko la Jamaica, Burning Spear, akubwera kudzayimba mdziko muno mwezi wa October chaka chino.
Akuluakulu omwe anakonza phwando la nyimbo la ku Mingoli Bash a Sound Addicts Live pamodzi ndi a Sound System Club ndi omwe akonza phwandoli ndipo atsimikiza zankhaniyi.
Aka kakhala koyamba kuti katswiriyu yemwe ali ndi zaka 79 adzayimbe ku Malawi.