Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

Bungwe la CARD lati MBC ndi akadaulo powulutsa mawu

Bungwe la Churches Action in Relief and Development (CARD) layamikira nyumba yowulutsa mawu ya Malawi Broadcasting Corporation (MBC) ponena kuti ndi akadaulo pantchito yawo.

Mkulu wa bungwe la CARD, a Melton Luhanga, ananena izi ku Blantyre pamene mabungwewa amasainirana mgwirizano wa chaka chimodzi.

Malinga ndi mgwirizanowo, MBC Idziwulutsa ma programme okhudza ntchito zimene bungwe la CARD limagwira kuphatikizirapo zaulimi komanso umoyo wabwino.

A Luhanga ati asankha kuchita mgwirizanowu chifukwa MBC imafikira penapaliponse komanso ili ndi akadaulo odziwa bwino ntchito yawo.

Mkulu oona zolemba anthu ntchito ku MBC, a Justice Matonga, anati mgwirizanowu ndi umboni okuti anthu ambiri ali ndi chikhulupiliro ndi wailesi ya MBC.

A Matonga anamema anthu ndi mabungwe kuti ndi olandiridwa kugwira ntchito ndi wailesiyi.

 

Related posts

First Lady in Geneva for TB Summit

Alinafe Mlamba

GESD Project launches K222 million Chilengo Health Post Construction

Romeo Umali

Seed strategy and investment plan launched

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.