M’buyomu: Ma Bishop a mpingo wakatolika ndi mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera.
Boma lati lipitiriza kuyankhulana komanso kumvana ndi ma Bishop a mpingo wa katolika pofuna kupititsa patsogolo miyoyo ya anthu m’dziko muno.
Mneneri wa boma, yemwenso ndi nduna yofalitsa nkhani, a Moses Kunkuyu, anena izi poyankhula ndi MBC potsatira kalata yomwe ma Bishop a Katolika atulutsa lamulungu.
Mu kalatayi, ma Bishopuwa apempha boma kuti lithetse mavuto osiyanasiyana omwe anthu akukumana nawo.
A Kunkuyu, mmau awo, ati boma lipitiriza kuyankhulana ndi ma Bishopuwa pomwenso akutsata njira zoyenera potukula chuma cha dziko lino ndi miyoyo ya anthu.