Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

Bambo mfumu alimbikitsa anthu kukhala olimbikira pa ntchito za Mulungu

Bambo mfumu Henry Zulu aku St. Patrick Parish ku Area 18 ati malemu Dr Saulos Chilima anali olimbikira pogwira ntchito zampingo komanso kutumikira dziko.

Iwowa anena izi pa mwambo wa misa ya maliro a wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko linoyu.

Pamwambowu panafika akuluakulu osiyanasiyana, kuphatikizapo woimira kampani ya Airtel yomwe Dr Chilima adagwirako ntchito, kudzanso nduna zaboma.

Pali chikonzero kuti tsiku lililonse kudzikhala mwambo wa misa katatu. Mwambo wa Misa wina uchitikanso 12 koloko masana komanso 6 koloko madzulo.

Dr Chilima adamwalira pa ngozi ya ndege yomwe adakwera itagwa mu nkhalango ya Chikangawa.

 

Related posts

MBC holds corruption and fraud awareness for staff

Alinafe Mlamba

MCCCI Business Leaders Summit receives boost from Britam Insurance

Alinafe Mlamba

MFC champions sustainable fertilizer usage in Malawi

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.