Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Awagwira komwe amabisala

Apolisi ku Soche mumzinda wa Blantyre amanga amuna ena awiri, kuphatikiza pa atatu omwe anawagwira kale mwezi wa March, pa mlandu wakuba ndikuvulaza munthu ku Soche East mumzinda womwewo.

Ofalitsankhani wapolisi ku Soche, Aaron Chilala, wati awiriwo, omwe awagwira ku Nsanje komwe amabisala, ndi John Washen wazaka 57 ndi James Basopa wazaka 37, ndipo awapezanso ndi zipolopolo 12.

A Chilala ati awiriwo, pamodzi ndi ena atatu omwe akuwasunga ku ndende ya Chichiri, anapita kunyumba ya Alex Makanjira ku Soche East, omwe anawaombera ndi mfuti yamtundu wa AK-47 kenako anaba katundu wa mnyumba ndi ndalama zokwana K100, 000.

Apolisi anakwanitsa kupeza katundu wina wobedwayo komanso anapeza mfuti yomwe anthuwo amagwiritsa ntchito.

Related posts

‘Nduna yayikulu ku UK idzigula yokha zovala, magalasi a maso’

Romeo Umali

Masamba ndi Tcheta afwafwanthana madzulo ano

Alinafe Mlamba

Dr. Chakwera wapepesa a Katolika pa imfa ya Papa

Blessings Kanache
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.