Nduna yazamalo a Deus Gumba atsindika kufunika kogwira ntchito limodzi ndi apolisi pantchito yolimbana ndi kuthetsa mikangano yokhudza malo m’dziko muno.
Ndunayi yanena izi ku Mponela m’boma la Dowa pa maphunziro ophunzitsa apolisi nkhani yokhudza kukonzedwanso kwa malamulo okhudza malo, komanso ndondomeko zokhudza malo.
A Gumba ati kugwira ntchito limodzi ndi apolisi kuthandiza kuti pasakhale chinyengo komanso mchitidwe olowelera malo, omwe akuti wakula m’dziko muno.
Iwo apemphaso apolisi kuti adziweruza mikangano yokhudza malo mopanda chinyengo.
Komishonala wa apolisi m’chigwawo cha pakati a Emmanuel Soko ati maphunzirowa athandizira kuti apolosi adzigwira ntchito yawo molingana ndi momwe malamulo alili.
Olemba : Madalitso Mhango