Malawi Broadcasting Corporation
Crime Development Local Local News

Apolisi apeza galimoto yobedwa

Apolisi ku Lilongwe apeza galimoto ya mtundu wa Nissan NP200 yomwe mbava zomwe sizikudziwika zinabera dotolo wina pa round about ya Mchinji mu msewu Bypass.

Ofalitsa nkhani ku Polisi ya Lilongwe, a Hastings Chigalu, ati izi zidachitika usiku wa pa 6 July pamene mwini galimotoyo amachokera ku Likuni kupita ku Area 47.

A Chigalu ati eni galimotowo anaima pambali pa msewu chifukwa galimoto yawo inatha mafuta ndipo akuba amene anatenga zikwanje anawakhapa ndi kuwabera galimoto koma sanapite nayo patali chifukwa apolisi amene amayendayenda m’deralo anafika pafupi ndipo mbalazo zidathawa.

Akuzungulirabe, apolisiwo anakumana ndi mwini galimotoyo ali magazi okhaokha uku akufuula kufuna chithandizo ndipo anamutenga ndi kumuuza kuti ayipeza.

Padakali pano, apolisiwo akuyang’anabe mbavazo zomwe zathawa ndi foni ya mtundu wa Itel ndi ndalama zokwana K7 thousand.

 

Related posts

Ntaja to open Eastern Region League

MBC Online

2024 SONA IN SYNC WITH MW 2063 — NPC

Alinafe Mlamba

MACRA’S CERT VOWS TO TACKLE CYBER THREATS

Alinafe Mlamba
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.