Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Politics

‘Anthu achikulire akhale ndi mwayi ovota’

Mtsogoleri wa chipani cha Alliance for Democracy (AFORD), a Enoch Chihana, apempha boma kuti pakhale ndondomeko zapadera zothandiza anthu achikulire kuti nawo adzapeze mwayi oponya voti m’zisankho za chaka cha mawa.

Iwo amanena izi pa msonkhano wa ndale omwe chipani chawo chidakonza mu mzinda wa Mzuzu Loweluka masana.

A Chihana ananenetsa zakufunikira kolimbikitsa anthu, kuphatikizapo achikulire, kuti alembetse mu kaundula wa unzika kuti akhale ndi ziphaso ndi cholinga chakuti anthu ochuluka adzakhale ndi mwayi ovota.

Olemba: Musase Cheyo

Related posts

President Chakwera to open Agriculture Investment Conference

Romeo Umali

POLICE  INVESTIGATING RECENT SPATE OF  MURDERS IN LL

MBC Online

Dr Usi amema ogwira ntchito m’boma kuti atsatire malonjezo a maiko olemera ku COP29

Alinafe Mlamba
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.