Ena mwa akatswiri oona zamalingaliro m’dziko muno ati pakufunika maphunziro ozindikiritsa ana osaposera zaka 13 momwe angadzitetezere kum’chitidwe wankhanza zogonana poyang’anira kukula kwa m’chitidwewu m’dziko muno.
M’modzi mwa akatswiriwa, Chiwoza Bandawe, wati ana omwe amatha kumvetsetsa zinthu apakati pa zaka 5 ndi 13 azindikiritsidwe kuti matupi awo sakuyenera kugwiridwa ndi munthu wina aliyense komanso aphunzitsidwe njira zodzitetezera, kuphatikizapo kukuwa, ngati munthu akuwagwira malo osayenera.
“Ndizomvetsa chisoni kuti anthu omwe amachita izi ndi anthu oti anawa amawakhulupilira chifukwa ambiri amakhala achibale oti akuyenera kuwateteza.
“Pali anthu ena omwe amaopa kufikira akuluakulu anzawo kuti achite nawo m’chitidwewu choncho amathawira kwa ana, zomwe ndikhalidwe loipa. Tiphunzitsenso mwana wamwamuna zakugonana kuti adzizindikira kuti akamva nthupi mwake kuti akufuna kugonana ndi munthu, njira zoyenera komanso malamulo amati chani,” watero Bandawe.
Povomerezana ndi a Bandawe, a Silvia Namakhwa a bungwe la Trust Psychosocial Support , ati anthu ena omwe amachita izi ndi anthu omwe anachitidwako nkhanza ali ang’ono ndipo sanathandizidwe kuthana ndi zovuta zomwe zimadza ndinkhanzazi.
Iwo anatinso pali anthu ena omwe amakhala ndichilakolako chogonana ndi ana achichepere okhaokha, kuphatikizapo zizimba zina zomwe ndizabodza. Iwo atsindika zaubwino othandiza anthu omwe amamangidwa pamilanduyi ndi ulangizi okonza malingaliro amunthu, kupatula kupereka chilango poganiza kuti munthu angasinthe.
Nkhani zogwililira ana zikuchulukira m’dziko muno pomwe sabata yapitayi abambo awiri azaka zoposa makumi asanu anjatidwa kamba kogwililira ana azaka zitatu, zisanu ndi zitatu komanso zisanu ndizinayi kungotchulapo milandu yochepa.
Olemba : Rashidah Matandika