Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

A Nankhumwa akana kulankhula mawu omaliza potsekera msonkhano wa aphungu

Mtsogoleri wa aphungu otsutsa boma ku Nyumba ya Malamulo, a Kondwani Nankhumwa, akana kulankhula mawu omaliza potsekera msonkhano wa aphunguwa, umene wakhala ukuchitika kwa sabata zisanu ndi zitatu.

Pamene Nyumba ya Malamulo ikumaliza  msonkhano wake lero, Sipikala wa Nyumbayi, a Catherine Gotani Hara, anapereka mpata kwa mkulu wa chipani cha DPP a Mary Navitcha kuti alankhule mau awo omaliza pa msonkhanowu, ndipo atamaliza, a Catherine Gotani Hara anaperekanso mpata kwa mtsogoleri wa aphungu otsutsa boma mnyumbayi kuti nawo alankhulepo

Koma a Nankhumwa anakana kulankhula ponena kuti zomwe sipikalayu wachita polora a Navitcha kulankhula ndizosemphana ndi malamulo.

Related posts

Tembo believes minerals can transform Malawi’s economy 

MBC Online

WANDERERS DISSOLVES SUPPORTERS BOARD 

Romeo Umali

DPP to complete infrastructure development in the North

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.