Apolisi ku Lilongwe amanga Jonas Sainani wazaka 45, pomuganizira kuti wapha mkazi wake wamkulu, Rosemary July wazaka 44.
Izi zachitika kunyumba kwa mkazi wake wang’ono.
Mneneri wapolisi ku Lilongwe, Hastings Chigalu, wati mkazi wamkuluyo anapita kunyumba kwa mkazi mnzake kuti akakambirane ndi mwamuna wake, yemwe panthawiyo anali komweko.
Kenaka ndewu inabuka kaamba kakusamvana.
Mwamunayo anatenga chitsulo ndikumenya mkazi wakeyo pamutu ndipo anagwa ndikukomoka.
Anthu ena anathamangira naye ku chipatala komwe anawauza kuti anali atamwalira.
Awiriwa akhala m’banja zaka 26 ndipo ali ndi ana asanu. Onse ndi a mmudzi wa Kaziputa m’boma la Lilongwe.