Khoti la Midima ku Limbe mumzinda wa Blantyre lalamula mayi Veronica Chakhumbira azaka 34 kuti alipire chindapusa cha ndalama zokwana K30, 000 chifukwa chotchula mzake kuti ndi mfiti pa masamba a mchezo.
Wachiwiri kwa ofalitsankhani zapolisi ku Limbe, Chibisa Mulimbika, wati mayi Chakhumbira analemba pa Facebook kuti mzawoyo ndi mfiti ndipo atawerenga, mzake wamayiyo anakanena izi ku polisi ya Bangwe ndipo apolisiwo anachenjeza mayiyo kuti alekeretu mchitidwewu.
Koma mayiyo anapitirizabe kutchula mayi mzakeyo kuti ndi mfiti, zomwe zinachititsa kuti apolisiwo amumange.
Mayi Chakhumbira ndi wa mmudzi wa Nkhanyanga, mfumu yaikulu Changata ku Thyolo.