Sukulu ya sekondale ya private ya Maranatha Academy ndi yomwe yatumiza chiwerengero chachikulu cha ana omwe awasankha kuti akayambe maphunziro aza ukachenjede kusukulu zosiyanasiyana m’dziko muno.
Malinga ndi zotsatira zomwe atulutsa a National Council for Higher Education (NCHE) dzulo ana okwana 246 ndi amene awasankha kuchokera ku sukulu ya Maranatha.
Polankhula ndi MBC, mkulu wa sukulu za Maranatha Academy, Enerst Kaonga, wati ndi okondwa kuti kwa zaka zingapo tsopano, sukulu yawo yakhala ikutumiza chiwerengero chochuluka cha ana ku sukulu za ukachenjede za m’dziko muno.
“… ndife okondwa kuti a NCHE awonetsa mtundu wa aMalawi kuti tili pa nambala 1 pa nkhani yosula ana, izi zakwaniritsidwa chifukwa cha khama lomwe aphunzitsi athu amayikapo pa ntchito yothetsa umbuli ndipo tikutsimikiza kuti tipitiliza kudzapeleka pa ntchito yathu”, atero a Kaonga.
Ana okwana 9,226 ndi omwe awasankha kuti akayambe maphunziro awo aza ukachenjede msukulu zisanu ndi imodzi za ukachenjede za boma m’dziko muno.
Simeon Boyce, MBC digital, Manthu