Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

RTCDT yati chakudya si nsima yokha

Komiti yagulu la nthambi zosiyanasiyana yoona za mbewu zazikhawo monga Chinangwa ndi Mbatata yati pakufunika kusintha maganizo pankhani ya chakudya chomwe dziko lino limadalira.

Wapampando wa komitiyi, a Jean Pankuku, wayankhula izi ku Lilongwe pomwe komitiyi imakumana ndi alimi komanso akuluakulu aku unduna wazaulimi.

“Tikufunika kuyika chidwi ku ulimi wa mbewu zotere chifukwa nyengo siikupanganika. Boma liganizire zoyika ndondomeko zazipangizo zotsika mtengo ku ulimi wazikhawo osati chimanga chokha,” atero a Pankuku.

M’modzi mwa akuluakulu ku unduna wa zaulimi, a Alfred Mwenefumbo, wati ndi zomvetsa chisoni kuti ambiri amatenga ulimiwu ngati chongophelera chabe pomwe mvula yachita njomba.

A Mwenefumbo apempha alimi kuti abwere pamodzi ndikuyamba kuchita ulimiwu pa mlingo waukulu ndikumapha makwacha kaamba koti misika ilipo kale yopezekeratu.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Usi atsekulira msonkhano okambirana za magetsi

MBC Online

MBC Socials yagonja 4-3 kwa Mablacks

Simeon Boyce

Khosolo ya Lilongwe yakhazikitsa komiti yoona za bata ndi mtendere

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.