Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera walamula kuti malemu a Raphael Kasambara ayikidwe m’manda potsatira mwambo wachisilikali.
Pakalinpano mwambo oika m’manda malemuwa uli mkati m’mudzi mwa Chijere m’boma la Nkhata Bay.
A Kasambara anali katswiri pa nkhani za malamulo ndipo anamwalira pa 7 June 2024 mu mzinda wa Lilongwe. Iwo anakhalaponso nduna yoona za malamulo komanso mkulu oyimira boma pa milandu (Attorney General) ndipo anabadwa m’chaka cha 1969.