Oyankhulapo pa nkhani za ndale a Undule Mwakasungula ati kuchoka kwa a Dalitso Kabambe ku chipani Democratic Progressive (DPP) kutha kukhala kukhumudwa chifukwa a Peter Mutharika, mtsogoleri wa chipanichi, m’mbuyomu adanenetsa kuti ayimira ngati mtsogoleri pa zisankho za chaka cha mawa.
A Kabambe m’mbuyomu akhala akuonetsa chidwi chofuna kudzayimira ngati mtsogoleri wa DPP.
A Mwakasungula alangiza a Kabambe, amene alengeza lero kuti achoka mu chipani cha DPP, kuti abwere poyera ndikufotokoza za kumene alowere komanso zimene achite.
Masana a Lolemba, a Kabambe, kudzera mu chikalata, anati iwo a choka m’chipanichi ataganizira mozama komanso anadziwitsa m’tsogoleri wa chipanichi, a Mutharika.
Ofalitsa nkhani ku DPP, a Shadric Namalomba, anakana kuyankhulapo pa nkhaniyi.
A Kabambe adagwirapo ntchito ngati gavanala wa Reserve Bank of Malawi.