Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Religion

M’busa apempha anthu kuti athandize osowa

Atsogoleri amipingo ati nkofunika kuti anthu adzipereka thandizo kwa iwo ovutika potsatira mavuto omwe ambiri m’dziko muno akukumana nawo.

M’busa Bishop William Mandhlopa a mpingo wa Family of God International anayankhula izi ku Area 44 mumzinda wa Lilongwe pamwambo opereka nyumba kwa bambo ndi mai George Phiri, amene ndi abusa opuma a mpingo wa Holy Ghost ndipo ndi okalamba.

Iwo anati chimene achitachi chikhale chilimbikitso kwa anthu kuti adzipereka thandizo kwa iwo ovutika.

M’mau awo, bambo ndi mai Phiri anayamika kwambiri m’busayo kaamba ka nyumbayi, ponena kuti moyo okhala pa rent unali ovuta.

Nyumbayo yamangidwa ndi ndalama zokwana K8 million.

#MBCOnlineServices

Related posts

Human Trafficking persists

Romeo Umali

Chakwera to inaugurate Magwero Industrial Park

Alinafe Mlamba

Education ministry eyes ODeL expansion as learner numbers rise

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.