Mtsogoleri wa bungwe loyang’anira sukulu zomwe sizaboma mdziko muno la Independent Schools Association of Malawi (ISAMA) a Wycliff Chimwendo ati ntchito yauphunzitsi ndi maitanidwe ndipo mphunzitsi wina aliyense akuyenera kudziwa kuti ntchito yawo siyopezera phindu la chuma kwenikweni.
A Chimwendo anena izi ku Lilongwe atayendera ophunzira omwe ali pa ndondomeko yophunzitsa aphunzitsi omwe amaphunzitsa ku sukulu zomwe sizaboma.
Malinga ndi a Chimwendo anakhazikitsa ntchito yophunzitsa aphunzitsiwa ati pogwirizana ndi boma pantchito yomwe likugwira lofuna kuonetsetsa kuti aphunzitsi onse mdziko muno ali ndi maphunziro oyenera ogwilira ntchito.
” Tithokoze kwambiri boma potipatsa mpata kuti aphunzitsi athu adzilandira ukadaulo pantchito yawo pamtengo oyenelera. Aphunzitsi ngakhare amagwira ntchito nwautumiki amayenera kukhara ndi ukadaulo oyenera pantchito yawo,” anatero a Chimwendo.
M’mawu ake mtsogoleri wa ophunzirawa pa sukulu ya Lilongwe Teachers Training College a Thomas James ati apindula kwambiri kudzera pandondomekoyi.
Iwo apemphanso ophunzira anzawo kuti ayesetse kugwiritsa ntchito luso lomwe aphunzira kuti lipindulire dziko lino.
Bungwe la ISAMA likuphunzitsa aphunzitsiwa kudzera pa ubale omwe linapanga ndi boma ndipo pakadali pano aphunzitsi a sukulu zamkombaphala akuphunzilira ku area 36 mu mzinda wa Lilongwe pomwe gulu lina likuphunzilira ku Blantyre Teachers Training College ndi ku Malawi Assemblies of God University ku Lilongwe ndipo ati posachedwapa ena aziphunzilanso ku Nalikule ndi Domasi Teachers College.

