Bungwe lomwe limayang’anira ntchito za masewera a mulosera la Malawi Gaming and Lotteries Authority (MAGLA) lati ntchito yolimbikitsa miyambo ya chikhalidwe ikuyenera kuthandiziridwa mokwanira pofuna kulimbikitsa komanso kuteteza mbiri ya dziko lino.
Mkulu oyendetsa ntchito za MAGLA a Lawrence Chikoko anena izi pomwe bungweli limapereka thandizo la ndalama zokwana K5 million ku bungwe la chikhalidwe la anthu a maboma a Karonga ndi Chitipa la Karonga, Chitipa Heritage Foundation zothandizira mwambo wa chikhalidwe otchedwa Karonga, Chitipa Cultural Festival omwe uchitike mwezi wa mawa.
A Chikoko ati chikhalidwe chimalimbikitsa mtendere komanso ntchito zokopa alendo zomwe zilinso ndikuthekera kokweza chuma cha dziko lino. Iwo ati choncho ndikofunika kuti kampani ndi ma bungwe osiyanasiyana adzipereke pothandizira ntchitoyi.
Wapampando wa bungwe la Karonga, Chitipa Heritage Foundation Marumbo Mwasinga wathokoza bungwe la MAGLA kaamba kathandizoli ponena kuti zalimbikitsa ntchito yotolera ndalama za mwambo wachakachinowu omwe ukufunika ndalama zokwana K50 million.
A Mwasinga ati sadafikirebe mulingowu ndipo apempha anthu ndi ma bungwe osiyanasiyana akufuna kabwino kuti athandize chikonzekerochi.
Mwambowu ukuyembekezeka kuchitika pa 18 mpaka pa 19 October ku phiri la Mbande m’boma la Karonga komwe kudzakhale magule, zakudya ndinso miyambo yosiyanasiyana ya anthu akuchitipa ndi Karonga.