Yemwe akufuna kudzayimira chipani cha Malawi Congress (MCP) pampando wa phungu kum’mwera m’boma la Ntcheu, a Joe Ching’ani, ati pakufunika kulimbikitsa maphunziro a sukulu za mkombaphala ngati njira imodzi yotukula maphunziro m’dziko muno.
Iwo amayankhula izi m’boma la Ntcheu pomwe amatsekulira sukulu ya mkombaphala ya Mwanang’ombe, yomwe ayimanga ndi ndalama pafupipafupi K7 miliyoni m’dera la mfumu yayikulu Phambala m’bomali.
Iwo ati akadzasankhidwa kukhala phungu waderali, adzapitiriza kupereka zitukuko zosiyanasiyana potsata mfundo za masomphenya a dziko lino a Malawi 2063, omwe mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera akulimbikitsa.
M’mawu ake, mfumu yayikulu Inkosi Phambala yati zomwe a Ching’ani apanga ndi zinthu zapamwamba.
Olemba: Thoccoh Jumpha