Yemwe amakhala pafupi ndi nyumba ya malemu “soldier” Lucius Banda m’boma la Balaka, Ras Jonah, yemwe dzina lake lenileni ndi Ronald Chigwale, wati mu nyimbo zake zambiri, malemu “soldier” mumakhalanso uthenga umene ma Rasta amakonda kupereka, monga kulakhulira anthuopondelezedwa, kulimbikitsa anthu kukhala olimbikira pa ntchito komanso kulimbikitsa chikondi.
Ras Jonah, yemwenso ndi oyimba, wati m’chaka cha 2002, malemu Lucius Banda anathandiza msonkhano wawo wawukulu wa ma Rasta ku Salima, kumene kunaabweranso oyimba akunja pamwambo wa zoimbaimba, umene ndalama zonse anazipeleka kukathandizira chilinganizochi.