Mphunzitsi wa timu yaikulu ya mpira wa miyendo m’dziko muno, Patrick Mabedi, wati waauza anyamata ake kuti mawa adzasewere ndicholinga chofuna kubwezeretsa ulemu kudziko lino komanso kupereka ulemu kwa amayi m’dziko muno pozindikira kuti ndi tsiku la anakubala.
Mabedi wanena izi pomwe timu ya Flames imachita zokonzekera zake pabwalo la Bingu munzinda wa Lilongwe.
Mabedi wati pali zambiri zomwe zinathandizira kuti timu ya Flames isachite bwino pa masewero omwe inagonja zigoli zinayi kwa duu ku Senegal, kuphatikizapo makonzekeredwe osakwanira komanso kupatsidwa red card kwa mnyamata otchinga pagolo, Brighton Munthali.
Koma iwo ati zonsenzi aziyika kumbuyo ndipo chidwi chonse chaikidwa popereka chimwemwe kwa aMalawi pamasewero a mawa.