Nthambi yowona za nyengo m’dziko muno yati mvula ikhala ikugwa mpakana sabata ya mawa, pamene yayamba kuvumba m’maboma ambiri kuyambira loweruka m’mawa.
Ena ati zimenezi zitha kupangitsa kuti mbewu zosiyanasiyana, zimene zinayamba kunyala chifukwa cha ng’amba, zitsitsimuke pamene mvula yagwa.
Kubwera kwa mvulaku kwaika chikhulupiliro mea ambiri kuti mwina alimi akhoza kukolora mokwanira, zimene zingathandize kupewa njala.