Mkulu wa MBC a George Kasakula ati malemu Geoffrey Kapusa anali munthu yemwe anali katakwe pantchito youlutsa mawu pa kanema komanso kuongolera tsogolo lankhani zoulutsa mawu pakanema m’dziko muno.
A Kasakula anena izi pamwambo oika m’manda a Kapusa, umene uli mkati kumudzi kwawo kwa malemwuwa.
Naye phungu wadera lakummwera kwa boma la Machinga, a Grant Ndecha, anati derali linali lokondwa kaamba kakuti linali ndi munthu yemwe achinyamata amadalira powalimbikitsa pa maphunziro kuti nawo adzakhale ndi ntchito yapamwamba.
MBC yakhala ikuthandiza a Kapusa kuyambira akudwala kufikira pano.