Mkulu wa apolisi m’dziko muno, a Merlyne Yolamu, wachenjeza kuti apolisi athana ndi wina aliyense oyambitsa ziwawa panthawi imene zokonzekera zachisankho zili mkati.
A Yolamu apereka chenjezoli pa msonkhano opereka uthenga olimbana ndi nkhanza zosiyanasiyana, omwe unachitikira m’boma la Mzimba pa Jenda.
“Ndichenjeze pano kuti timanga wina aliyense oyambitsa zisokonezo nthawi ino, lolani wina aliyense apange msonkhano wake mwaufulu posazulirana mbendera kapena kemenyana,” anatero a Yolamu.
Iwo anati a Malawi ndi amodzi ngakhale amasiyana zipani kotero anthu sakuyenera kusankhana.
Olemba: Henry Haukeya